Mangochi ndi mzinda omwe uli ku m'mwela kwa kwa dziko la Malawi.
Mzindawu uli ku mapetopeto a ku m'wela a Lake Malawi. Mu nthawi ya atsamunda mzindawu unkadziwika ndi dzina lokuti Fort Johnstone. Kumathero kwa chaka cha 2008 mu mzinda wa Mangochi munali anthu pafupifupi 51,429.
Mangochi ndi mzinda omwe udayambitsidwa ndi bwana m'kubwa a chitsamunda Sir Harry Johnston mu zaka za'ma 1890s ngati doko la chitetezo la atsamunda cha ku madzulo m'phepete mwa mstinge wa Shire Kuchokera apa Fort Johnston – monga unkadziwikila mzindawu pa nthawiyi –udali mzinda omwe kunkayendetsedwa nkhani zokhudzana ndi kugulistidwa kwa anthu okagwira ntchito ya kalavula gaga m'mayiko a ku ulaya, komanso mzindawu unkagwira ntchito ngati koyendetserako boma la atsamunda.
This article uses material from the Wikipedia Chichewa article Mangochi, which is released under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 3.0 license ("CC BY-SA 3.0"); additional terms may apply (view authors). Content is available under CC BY-SA 4.0 unless otherwise noted. Images, videos and audio are available under their respective licenses.
®Wikipedia is a registered trademark of the Wiki Foundation, Inc. Wiki Chichewa (DUHOCTRUNGQUOC.VN) is an independent company and has no affiliation with Wiki Foundation.